Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 9:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Sandilola kuti ndipume,Koma andidzaza ndi zowawa.

19. Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu?Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?

20. Cinkana ndikhala wolungama, pakamwa panga padzanditsutsa;Cinkana ndikhala wangwiro, padzanditsutsa wamphulupulu.

21. Cinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini,Ndipeputsa moyo wanga.

22. Kuli cimodzimodzi monsemo, m'mwemo ndikutiIye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.

23. Mkwapulo ukapha modzidzimutsa,Adzaseka tsoka la wosacimwa.

24. Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa;Aphimba maso a oweruza ace.Ngati sindiye, pali yaninso?

25. Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma;Athawa osaona cokoma.

26. Apitirira ngati zombo zaliwiro;Ngati mphungu igudukira cakudya cace.

27. Ndikati, Ndidzaiwala condidandaulitsa,Ndidzasintha nkhope yanga yacisoni, ndidzasekerera;

28. Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse,Ndidziwa kuti simudzandiyesa wosacimwa.

29. Mlandu udzanditsutsa;Potero ndigwire nchito cabe cifukwa ninji?

Werengani mutu wathunthu Yobu 9