Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 8:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,Popeza masiku athu a pa dziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10. Amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,Ndi kuturutsa mau a mumtima mwao?

11. Ngati gumbwa aphuka popanda cinyontho?Ngati mancedza amera popanda madzi?

12. Akali auwisi, sanawaceka,Auma, asanaume mathengo onse ena.

13. Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;Ndi ciyembekezo ca onyoza Mulungu cidzatayika;

14. Kulimbika mtima kwace kudzatyoka,Cikhulupiriro cace cikunga nyumba ya tandaude.

15. Adzatsamira nyumba yace, koma yosamlimbira;Adzaiumirira koma yosakhalitsa.

16. Akhala wamuwisi pali dzuwa,Ndi nthambi zace ziturukira pamunda pace.

Werengani mutu wathunthu Yobu 8