Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 8:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,

2. Udzanena izi kufikira liti?Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

3. Ngati Mulungu akhotetsa ciweruzo?Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?

4. Cinkana ana ako anamcimwira Iye,Ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;

5. Koma ukafunitsitsa Mulungu,Ndi kupembedza Wamphamvuyonse;

6. Ukakhala woyera ndi woongoka mtima,Zoonadi adzakugalamukira tsopano,Ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.

7. Ndipo cinkana ciyambi cako cinali cacing'ono,Citsiriziro cako cidzacuruka kwambiri.

8. Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo,Nusamalire zimene makolo ao adazisanthula;

9. Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,Popeza masiku athu a pa dziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10. Amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,Ndi kuturutsa mau a mumtima mwao?

Werengani mutu wathunthu Yobu 8