Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 7:3-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pace.Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.

4. Ndigona pansi, ndikuti,Ndidzauka liti? koma usiku undikulira;Ndipo ndimapalapata mpaka mbanda kuca.

5. Mnofu wanga wabvala mphutsi ndi nkanambo zadothi;Khungu langa lang'ambika, nilinyansa.

6. Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,Apitirira opanda ciyembekezo.

7. Kumbukila kuti moyo wanga ndiwo mphepo,Diso langa silidzaonanso cokoma.

8. Diso la amene andiona silidzandionanso,Maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.

9. Mtambo wapita watha,Momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.

10. Sadzabweranso ku nyumba yace,Osamdziwanso malo ace.

11. Potero sindidzaletsa pakamwa panga;Ndidzalankhula popsinjika mumzimu mwanga;Ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.

12. Ndine nyanja kodi, kapena cinjoka ca m'nyanja,Kuti Inu mundiikira odikira?

13. Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,Pogona panga padzacepsa condidandaulitsa;

14. Pamenepo mundiopsa ndi maloto,Nimundicititsa mantha ndi masomphenya;

15. Potero moyo wanga usankha kupotedwa,Ndi imfa, koposa mafupa anga awa.

Werengani mutu wathunthu Yobu 7