24. Mundilangize, ndipo ndidzakhala cete ine;Mundizindikiritse umo ndinalakwira.
25. Mau oongoka si ndiwo amphamvu?Koma kudzudzula kwanu mudzudzula ciani?
26. Kodi muyesa kudzudzula mau?Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.
27. Indetu, mugwetsera wamasiye msampha,Mumkumbira bwenzi lanu mbuna.
28. Koma tsopano balindani, mundipenyerere;Ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.
29. Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu;Inde, bwereraninso, mlandu wanga ngwolungama.
30. Kodi pali cosalungama palilime panga?Ngati sindizindikira zopanda pace m'kamwa mwanga?