Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 6:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Yobu anayankha, nati,

2. Mwenzi atayesa bwino cisoni canga,Ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!

3. Pakuti zikadalemera tsopano koposa mcenga wa kunyanja;Cifukwa cace mau anga ndasonthokera kunena.

4. Pakuti mibvi ya Wamphamvuyonse yandilowa,Mzimu wanga uumwa ulembe wace;Zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.

5. Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu?Ilira kodi ng'ombe pa cakudya cace?

6. Kodi cinthu cosakolera cidyeka copanda mcere?Coyera ca dzira cikolera kodi?

7. Zimene moyo wanga ukana kuzikhudzaZikunga cakudya cosakolera kwa ine.

8. Ha! ndikadakhala naco cimene ndicipempha,Mulungu akadandipatsa cimene ndicilira!

9. Cimkomere Mulungu kundiphwanya,Alole dzanja lace lindilikhel

10. Pamenepo ndidzasangalala,Ndidzakondwera naco cowawa cosandileka;Pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo.

Werengani mutu wathunthu Yobu 6