Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 5:3-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndinapenya wopusa woyala mizu;Koma pomwepo ndinatemberera pokhala pace.

4. Ana ace akhala otekeseka, Napsinjika kucipata,Wopanda wina wakuwapulumutsa.

5. Zokolola zao anjala azidya,Azitenga ngakhale kuminga,Ndi aludzu ameza cuma cao.

6. Pakuti nsautso siituruka m'pfumbi,Ndi mabvuto saphuka m'nthaka;

7. Koma munthu abadwira mabvuto,Monga mbaliwali zikwera ziuluzika.

8. Koma ine ndikadafuna Mulungu,Ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;

9. Amene acita zazikuru ndi zosalondoleka,Zinthu zodabwiza zosawerengeka.

10. Amene abvumbitsa mvula panthaka,Natumiza madzi paminda;

11. Kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka,Kuti iwo a maliro akwezedwe posatekeseka.

12. Apititsa pacabe ziwembu za ocenjerera,Kuti manja ao sakhoza kucita copangana cao.

13. Akola eni nzeru m'kucenjerera kwao,Ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pacabe,

14. Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa,Nayambasa dzuwa liri pakati pamtu monga usiku.

15. Apulumutsa aumphawi ku lopangaLa kukamwa kwao, ndi ku dzanja la wamphamvu.

16. Potero aumphawi ali naco ciyembekezo,Ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.

17. Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula;Cifukwa cace usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.

18. Pakuti apweteka, namanganso mabala;Alasa, ndi manja ace omwe apoletsa.

19. Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi;Cinkana mwa asanu ndi awiri palibe coipa cidzakukhudza.

20. Adzakuombola kuimfa m'njala,Ndi ku mphamvu ya lupanga m'nkhondo.

Werengani mutu wathunthu Yobu 5