Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 5:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi;Cinkana mwa asanu ndi awiri palibe coipa cidzakukhudza.

20. Adzakuombola kuimfa m'njala,Ndi ku mphamvu ya lupanga m'nkhondo.

21. Udzabisikira mkwapulo wa lilime,Sudzaciopanso cikadza cipasuko.

22. Cipasuko ndi njala udzaziseka;Ngakhale zirombo za padziko osaziopa.

23. Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala ya kuthengo;Ndi nyama za kuthengo zidzakhala nawe mumtendere.

24. Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere;Nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu,

25. Udzapezanso kuti mbeu zako zidzacuruka,Ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.

26. Udzafika kumanda utakalamba,Monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yace.

27. Taona, ici tacifunafuna, ciri catero;Ucimvere, nucidziwire wekha.

Werengani mutu wathunthu Yobu 5