Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 41:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kodi idzapangana ndi iwe,Kuti uitenge ikhale kapolo wako wacikhalire?

5. Kodi udzasewera nayo ngati mbalame?Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?

6. Kodi opangana malonda adzaitsatsa?Adzaigawana eni malonda?

7. Kodi udzadzaza khungu lace ndi nchetho,Kapena mutu wace ndi miomba?

8. Isanjike dzanja lako;Ukakumbukila nkhondoyi, sudzateronso.

9. Taona, ciyembekezo cako ca pa iyo cipita pacabe.Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?

10. Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?

11. Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze?Ziri zonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.

12. Sindikhala cete osachula ziwalo za ng'onayo,Ndi mbiri ya mphamvu yace, ndi makonzedwe ace okoma.

13. Ndani adzasenda cobvala cace cakunja?Adzalowa ndani ku mizere iwiri ya mano ace?

14. Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pace?Mano ace aopsa pozungulira pao.

Werengani mutu wathunthu Yobu 41