Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 41:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kodi ukhoza kukoka ng'ona ndi mbedza?Kapena kukanikiza kalandira wace ndi cingwe?

2. Kodi ukhoza kumanga m'mphuno ndi mlulu?Kapena kuboola nsagwada wace ndi momba?

3. Kodi idzacurukitsa mau akukupembedza?Kapena idzanena nawe mau ofatsa?

4. Kodi idzapangana ndi iwe,Kuti uitenge ikhale kapolo wako wacikhalire?

5. Kodi udzasewera nayo ngati mbalame?Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?

6. Kodi opangana malonda adzaitsatsa?Adzaigawana eni malonda?

7. Kodi udzadzaza khungu lace ndi nchetho,Kapena mutu wace ndi miomba?

8. Isanjike dzanja lako;Ukakumbukila nkhondoyi, sudzateronso.

9. Taona, ciyembekezo cako ca pa iyo cipita pacabe.Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?

10. Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?

11. Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze?Ziri zonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.

12. Sindikhala cete osachula ziwalo za ng'onayo,Ndi mbiri ya mphamvu yace, ndi makonzedwe ace okoma.

Werengani mutu wathunthu Yobu 41