Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 40:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Cingakhale ciweruzo canga udzacityola kodi?Udzanditsutsa kuti ndiri woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?

9. Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?

10. Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika,Nubvale ulemu ndi ulemerero.

11. Tsanulira mkwiyo wako wosefuka,Nupenyerere ali yense wodzikuza ndi kumcepetsa,

12. Upenyerere ali yense wodzikuza, numtsitse,Nupondereze oipa pomwe akhala.

13. Uwakwirire pamodzi m'pfumbi,Uzimange nkhope zao pobisika.

14. Pamenepo inenso ndidzakubvomereza,Kuti dzanja lako lako lamanja likupulumutsa.

15. Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe,Ikudya udzu ngati ng'ombe.

16. Tapenya tsono, mphamvu yace iri m'cuuno mwace,Ndi kulimbalimba kwace kuli m'mitsempha ya m'mimba yace.

17. Igwedeza mcira wace ngati mkungudza;Mitsempha ya ncafu zace ipotana.

Werengani mutu wathunthu Yobu 40