Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 40:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Tapenya tsono, mphamvu yace iri m'cuuno mwace,Ndi kulimbalimba kwace kuli m'mitsempha ya m'mimba yace.

17. Igwedeza mcira wace ngati mkungudza;Mitsempha ya ncafu zace ipotana.

18. Mafupa ace akunga misiwe yamkuwa;Ziwalo zace zikunga zitsulo zamphumphu,

19. Iyo ndiyo ciyambi ca macitidwe a Mulungu;Wakuilenga anaininkha lupanga lace.

20. Pakuti mapiri aiphukitsira cakudya,Kumene zisewera nyama zonse za kuthengo,

21. Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,Pobisala pabango ndi pathawale.

22. Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao,Misondodzi ya kumtsinje iizinga.

23. Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera;Ilimbika mtima, ngakhale Yordano atupa mpaka pakamwa pace,

Werengani mutu wathunthu Yobu 40