Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 40:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati,

2. Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?Wocita makani ndi Mulungu ayankhe.

3. Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati,

4. Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?Ndigwira pakamwa.

5. Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;Inde kawiri, koma sindionjezanso.

6. Ndipo Yehova anamyankha Yobu m'kabvumvulu, nati,

7. Dzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna;Ndidzakufunsa, undidziwitse.

8. Cingakhale ciweruzo canga udzacityola kodi?Udzanditsutsa kuti ndiri woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?

9. Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?

Werengani mutu wathunthu Yobu 40