8. Monga umo ndaonera, olimira mphulupulu,Nabzala bvuto, akololapo zomwezo.
9. Atayika ndi mpweya wa Mulungu,Nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wace.
10. Kubangula kwa mkango, ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,Ndi mano a misona ya mkango atyoledwa.
11. Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,Ndi misona ya mkango waukazi imwazika.
12. Anditengera mau m'tseri,M'khutu mwanga ndinalandira kunong'oneza kwace.
13. M'malingaliro a masomphenya a usiku,Powagwira anthu tulo tatikuru,
14. Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,Nanthunthumira nako mafupa anga onse.
15. Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;Tsitsi la thupi langa lidati nyau nyau.
16. Unaima ciriri, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ace;Panali mzukwa pamaso panga;Kunali cete, ndipo ndidamva mau akuti,
17. Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wace?
18. Taona, sakhulupirira atumiki ace;Nawanenera amithenga ace zopusa;
19. Kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi,Amene kuzika kwao kuti m'pfumbi,Angothudzulidwa ngati gulugufe,
20. Kuyambira m'mawa kufikira madzulo athudzuka;Aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.
21. Kukometsetsa kwao sikumacotsedwa nao?Amafa koma opanda nzeru.