Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 4:2-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Munthu akayesa kunena nawe mau, kodi udzamva nao cisoni?Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?

3. Taona iwe walangiza aunyinji,Walimbitsa manja a ofoka.

4. Mau ako anacirikiza iye amene akadagwa,Walimbitsanso maondo otewa.

5. Koma tsopano cakufikira iwe, ndipo ukomoka;Cikukhudza, ndipo ubvutika.

6. Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,Ndi ciyembekezo cako si ndiwo ungwiro wa njira zako?

7. Takumbukila tsopano, watayika ndani wosaparamula konse?Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?

8. Monga umo ndaonera, olimira mphulupulu,Nabzala bvuto, akololapo zomwezo.

9. Atayika ndi mpweya wa Mulungu,Nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wace.

10. Kubangula kwa mkango, ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,Ndi mano a misona ya mkango atyoledwa.

11. Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,Ndi misona ya mkango waukazi imwazika.

12. Anditengera mau m'tseri,M'khutu mwanga ndinalandira kunong'oneza kwace.

13. M'malingaliro a masomphenya a usiku,Powagwira anthu tulo tatikuru,

14. Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,Nanthunthumira nako mafupa anga onse.

15. Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;Tsitsi la thupi langa lidati nyau nyau.

Werengani mutu wathunthu Yobu 4