Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 39:9-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kodi njati idzabvomera kukutumikira,Idzakhala ku codyetseramo cako kodi?

10. Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lace ilime m'mcera?Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa?

11. Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yace njaikuru?Udzaisiyira nchito yako kodi?

12. Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako,Ndi kuzisonkhanitsira kudwale?

13. Phiko la nthiwatiwa likondwera,Koma mapiko ndi nthenga zace nzofatsa kodi?

14. Pakuti isiya mazira ace panthaka,Nimafunditsa m'pfumbi,

15. Niiwala kuti phazi lingawaphwanye,Kapena cirombo cingawapondereze.

16. Iumira mtima ana ace monga ngati sali ace;Idzilemetsa ndi nchito cabe, popeza iribe mantha;

17. Pakuti Mulungu anaimana nzeru,Ndipo sanaigawira luntha.

18. Ikafika nthawi yace, iweramuka,Iseka kavalo ndi wa pamsana pace.

19. Wampatsa kavalo mphamvu yace kodi?Wambveka pakhosi pace cenjerere cogwedezeka?

20. Wamlumphitsa kodi ngati dzombe?Ulemerero wa kumina kwace ngwoopsa.

21. Apalasa kucigwa, nakondwera nayo mphamvu yace;Aturuka kukomana nao eni zida.

22. Aseka mantha osaopsedwa,Osabwerera kuthawa lupanga.

23. Phodo likuti koco koco panthiti pace,Mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe.

Werengani mutu wathunthu Yobu 39