Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 39:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Aseka phokoso la kumudzi,Osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli.

8. Poyenda ponse pamapiri mpa busa pace;Ilondola caciwisi ciri conse.

9. Kodi njati idzabvomera kukutumikira,Idzakhala ku codyetseramo cako kodi?

10. Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lace ilime m'mcera?Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa?

11. Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yace njaikuru?Udzaisiyira nchito yako kodi?

12. Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako,Ndi kuzisonkhanitsira kudwale?

13. Phiko la nthiwatiwa likondwera,Koma mapiko ndi nthenga zace nzofatsa kodi?

14. Pakuti isiya mazira ace panthaka,Nimafunditsa m'pfumbi,

15. Niiwala kuti phazi lingawaphwanye,Kapena cirombo cingawapondereze.

Werengani mutu wathunthu Yobu 39