Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 39:13-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Phiko la nthiwatiwa likondwera,Koma mapiko ndi nthenga zace nzofatsa kodi?

14. Pakuti isiya mazira ace panthaka,Nimafunditsa m'pfumbi,

15. Niiwala kuti phazi lingawaphwanye,Kapena cirombo cingawapondereze.

16. Iumira mtima ana ace monga ngati sali ace;Idzilemetsa ndi nchito cabe, popeza iribe mantha;

17. Pakuti Mulungu anaimana nzeru,Ndipo sanaigawira luntha.

18. Ikafika nthawi yace, iweramuka,Iseka kavalo ndi wa pamsana pace.

19. Wampatsa kavalo mphamvu yace kodi?Wambveka pakhosi pace cenjerere cogwedezeka?

20. Wamlumphitsa kodi ngati dzombe?Ulemerero wa kumina kwace ngwoopsa.

21. Apalasa kucigwa, nakondwera nayo mphamvu yace;Aturuka kukomana nao eni zida.

22. Aseka mantha osaopsedwa,Osabwerera kuthawa lupanga.

23. Phodo likuti koco koco panthiti pace,Mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe.

24. Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka,Osaimitsika pomveka lipenga.

25. Pomveka lipenga akuti, Hee!Anunkhiza nkhondo irikudza kutaliKugunda kwa akazembe ndi kuhahaza,

26. Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako,Natambasula mapiko ace kumka kumwera?

27. Kodi ciombankhanga cikwera m'mwamba pocilamulira iwe,Nicimanga cisanja cace m'mwamba?

28. Kwao nku thanthwe, cigona komweko,Pansonga pa thanthwe pokhazikikapo.

29. Pokhala kumeneko ciyang'ana cakudya;Maso ace acipenyetsetsa ciri kutali,

Werengani mutu wathunthu Yobu 39