Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 39:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma?Kodi wapenyerera pakuswa nswala?

2. Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira,Kapena udziwa nyengo yoti ziswane?

3. Zithuntha, ziswa,Zitaya zowawa zao.

4. Ana ao akhala ojinca, akulira kuthengo,Acoka osabwerera kwa amao.

5. Ndani walola mbidzi ituruke yaufulu?Anaimasulira mbidzi nsinga zace ndani,

6. Imene ndaciyesa cipululu nyumba yace,Ndi dziko lakhulo pokhala pace?

7. Aseka phokoso la kumudzi,Osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli.

8. Poyenda ponse pamapiri mpa busa pace;Ilondola caciwisi ciri conse.

9. Kodi njati idzabvomera kukutumikira,Idzakhala ku codyetseramo cako kodi?

Werengani mutu wathunthu Yobu 39