Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 38:5-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Analemba malire ace ndani, papeza udziwa?Anayesapo cingwe cace ndani?

6. Maziko ace anakumbidwa pa ciani?Kapena anaika ndani mwala wace wa pangondya,

7. Muja nyenyezi za m'mawa zinayimba limodzi mokondwera,Ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi cimwemwe?

8. Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko,Muja idakamula ngati kuturuka m'mimba,

9. Muja ndinayesa mtambo cobvala cace,Ndi mdima wa bii nsaru yace yakulunga,

10. Ndi kuilembera malire anga,Ndi kuika mipikizo ndi zitseko,

11. Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?

12. Kodi walamulira m'mawa ciyambire masiku ako,Ndi kudziwitsa mbanda kuca malo ace;

13. Kuti agwire malekezero a dziko lapansi,Nakutumule oipa acokeko?

14. Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa cosindikiza,Ndi zonse zibuka ngati cobvala;

15. Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.

16. Kodi unalowa magwero a nyanja?Kodi unayendayenda pozama peni peni?

17. Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe?Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?

18. Kodi unazindikira citando ca dziko lapansi?Fotokozera, ngati ucidziwa conse.

19. Iri kuti njira yomukira pokhala kuunika?Ndi mdima, pokhala pace pali kuti,

20. Kuti upite nao ku malire ace,Kuti uzindikire miseu ya ku nyumba yace?

21. Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo,Ndi masiku ako acuruka kuwerenga kwao.

Werengani mutu wathunthu Yobu 38