Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 38:26-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Kubvumbitsa mvula pa dziko lapanda anthu,Ku cipululu kosakhala munthu,

27. Kukhutitsa thengo la kunkhwangwala,Ndi kuphukitsa msipu?

28. Kodi mvula iri naye atate?Kapena wabala ndani madontho amame?

29. Cipale cinaturuka m'inimba ya yani?Ndi cisanu cocokera m'mwamba anacibala ndani?

30. Madzi aundana ngati mwala,Ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.

31. Kodi ungamange gulu la Nsangwe?Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?

32. Ungaturutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao?Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ace?

33. Kodi udziwa malemba a kuthambo?Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi?

34. Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo,Kuti madzi ocuruka akukute?

35. Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke,Ndi kunena nawe, Tiri pano?

36. Ndani analonga nzeru m'mitambomo?Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha?

37. Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru,Ndi kutsanulira micenje ya kuthambo ndani,

38. Pokandika pfumbi,Ndi kuundana zibuma pamodzi?

39. Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama?Ndi kukwaniritsa cakudya ca misona,

Werengani mutu wathunthu Yobu 38