Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 38:25-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndani anacikumbira mcera cimvula,Kapena njira ya bingu la mphezi,

26. Kubvumbitsa mvula pa dziko lapanda anthu,Ku cipululu kosakhala munthu,

27. Kukhutitsa thengo la kunkhwangwala,Ndi kuphukitsa msipu?

28. Kodi mvula iri naye atate?Kapena wabala ndani madontho amame?

29. Cipale cinaturuka m'inimba ya yani?Ndi cisanu cocokera m'mwamba anacibala ndani?

30. Madzi aundana ngati mwala,Ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.

31. Kodi ungamange gulu la Nsangwe?Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?

32. Ungaturutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao?Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ace?

33. Kodi udziwa malemba a kuthambo?Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi?

Werengani mutu wathunthu Yobu 38