Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 38:15-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.

16. Kodi unalowa magwero a nyanja?Kodi unayendayenda pozama peni peni?

17. Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe?Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?

18. Kodi unazindikira citando ca dziko lapansi?Fotokozera, ngati ucidziwa conse.

19. Iri kuti njira yomukira pokhala kuunika?Ndi mdima, pokhala pace pali kuti,

20. Kuti upite nao ku malire ace,Kuti uzindikire miseu ya ku nyumba yace?

21. Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo,Ndi masiku ako acuruka kuwerenga kwao.

22. Kodi unalowa m'zosungiramo cipale cofewa?Kapena unapenya zosungiramo matalala,

23. Amene ndiwasungira tsiku la nsautso,Tsiku lakulimbana nkhondo?

24. Njira iri kuti yomukira pogawikana kuunika,Kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa pa dziko lapansi?

25. Ndani anacikumbira mcera cimvula,Kapena njira ya bingu la mphezi,

26. Kubvumbitsa mvula pa dziko lapanda anthu,Ku cipululu kosakhala munthu,

27. Kukhutitsa thengo la kunkhwangwala,Ndi kuphukitsa msipu?

28. Kodi mvula iri naye atate?Kapena wabala ndani madontho amame?

29. Cipale cinaturuka m'inimba ya yani?Ndi cisanu cocokera m'mwamba anacibala ndani?

30. Madzi aundana ngati mwala,Ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.

31. Kodi ungamange gulu la Nsangwe?Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?

32. Ungaturutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao?Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ace?

33. Kodi udziwa malemba a kuthambo?Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi?

34. Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo,Kuti madzi ocuruka akukute?

35. Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke,Ndi kunena nawe, Tiri pano?

Werengani mutu wathunthu Yobu 38