Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 37:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. M'cipinda mwace muturuka kabvumvulu,Ndi cisanu cifuma kumpoto.

10. Mwa kupuma kwace apereka cipale,Ndi madzi acitando aundana.

11. Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi,Afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yace;

12. Ndipo utembenuka-tembenuka pakulangiza kwace,Kuti ucite ziri zonse aulamulira,Pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu;

13. Ngati aufikitsira dziko lace kulidzudzula,Kapena kulicitira cifundo.

14. Tamverani ici, Yobu.Taimani, mulingirire zodabwiza za Mulungu.

15. Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi,Nawalitsa mphezi ya m'mtambo mwace?

16. Kodi mudziwa madendekeredwe ace a mitambo,Zodabwiza za Iye wakudziwa mwangwiro?

17. Kodi mudziwa umo zobvala zanu zifundira,Pamene dziko liri thuu cifukwa ca mwela?

18. Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye,Ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka?

19. Mutilangize cimene tidzanena ndi Iye;Sitidziwa kulongosola mau athu cifukwa ca mdima.

Werengani mutu wathunthu Yobu 37