Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 37:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Akumveketsa pansi pa thambo ponse,Nang'anipitsa mphezi yace ku malekezero a dziko lapansi.

4. Mau abuma kuitsata,Agunda ndi mau a ukulu wace,Ndipo sailetsa atamveka mau ace,

5. Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ace,Acita zazikuru osazidziwa ife.

6. Pakuti anena kwa cipale cofewa, Ugwe padziko.Momwemonso kwa mvula,Ndi kwa mbvumbi waukuru.

7. Atsekereza mokhomera cizindikilo dzanja la munthu ali yense,Kuti anthu onse anawalenga adziwe.

8. Pamenepo zirombo zilowa mobisalamo,Nizikhala m'ngaka mwao.

9. M'cipinda mwace muturuka kabvumvulu,Ndi cisanu cifuma kumpoto.

10. Mwa kupuma kwace apereka cipale,Ndi madzi acitando aundana.

11. Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi,Afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yace;

12. Ndipo utembenuka-tembenuka pakulangiza kwace,Kuti ucite ziri zonse aulamulira,Pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu;

Werengani mutu wathunthu Yobu 37