1. Pa icinso mtima wanga unienjemera,Nusunthika m'malo mwace.
2. Mvetsetsani cibumo ca mau ace,Ndi kugunda koturuka m'kamwa mwace.
3. Akumveketsa pansi pa thambo ponse,Nang'anipitsa mphezi yace ku malekezero a dziko lapansi.
4. Mau abuma kuitsata,Agunda ndi mau a ukulu wace,Ndipo sailetsa atamveka mau ace,
5. Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ace,Acita zazikuru osazidziwa ife.
6. Pakuti anena kwa cipale cofewa, Ugwe padziko.Momwemonso kwa mvula,Ndi kwa mbvumbi waukuru.