Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 36:22-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace,Mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23. Anamuikira njira yace ndani?Adzati ndani, Mwacita cosalungama?

24. Kumbukilani kuti mukuze nchito zace,Zimene anaziyimbira anthu.

25. Anthu onse azipenyerera,Anthu aziyang'anira kutali.

26. Taonani, Mulungu ndiye wamkuru, ndipo sitimdziwa;Ciwerengo ca zaka zace ncosasanthulika.

Werengani mutu wathunthu Yobu 36