Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 36:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Cuma canu cidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,Kapena mphamvu yanu yonse yolimba?

20. Musakhumbe usiku,Umene anthu alikhidwe m'malo mwao.

21. Cenjerani, musaluniike kumphulupulu;Pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22. Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace,Mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23. Anamuikira njira yace ndani?Adzati ndani, Mwacita cosalungama?

24. Kumbukilani kuti mukuze nchito zace,Zimene anaziyimbira anthu.

25. Anthu onse azipenyerera,Anthu aziyang'anira kutali.

26. Taonani, Mulungu ndiye wamkuru, ndipo sitimdziwa;Ciwerengo ca zaka zace ncosasanthulika.

27. Pakuti akweza madontho a mvula,Akhetsa mvula ya m'nkhungu yace

Werengani mutu wathunthu Yobu 36