Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 36:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti mucenjere, mkwiyo ungakunyengeni mucite mnyozo;Ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.

19. Cuma canu cidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,Kapena mphamvu yanu yonse yolimba?

20. Musakhumbe usiku,Umene anthu alikhidwe m'malo mwao.

21. Cenjerani, musaluniike kumphulupulu;Pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22. Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace,Mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23. Anamuikira njira yace ndani?Adzati ndani, Mwacita cosalungama?

24. Kumbukilani kuti mukuze nchito zace,Zimene anaziyimbira anthu.

25. Anthu onse azipenyerera,Anthu aziyang'anira kutali.

26. Taonani, Mulungu ndiye wamkuru, ndipo sitimdziwa;Ciwerengo ca zaka zace ncosasanthulika.

27. Pakuti akweza madontho a mvula,Akhetsa mvula ya m'nkhungu yace

28. Imene mitambo itsanulira,Nibvumbitsira anthu mocuruka.

29. Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo,Ndi kugunda kwa msasa wace?

30. Taonani, Iye ayala kuunika kwace pamenepo.Nabvundikira kunsi kwace kwa nyanja.

Werengani mutu wathunthu Yobu 36