Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 36:12-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga,Nadzatsirizika osadziwa kanthu.

13. Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo,Akawamanga Iye, sapfuulira.

14. Iwowa akufa akali biriwiri,Ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.

15. Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwace,Nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao.

16. Inde akadakukopani mucoke posaukira,Mulowe kucitando kopanda copsinja;Ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.

17. Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa,Zolingirirazo ndi ciweruzo zidzakugwiranibe,

18. Pakuti mucenjere, mkwiyo ungakunyengeni mucite mnyozo;Ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.

19. Cuma canu cidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,Kapena mphamvu yanu yonse yolimba?

20. Musakhumbe usiku,Umene anthu alikhidwe m'malo mwao.

21. Cenjerani, musaluniike kumphulupulu;Pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22. Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace,Mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23. Anamuikira njira yace ndani?Adzati ndani, Mwacita cosalungama?

24. Kumbukilani kuti mukuze nchito zace,Zimene anaziyimbira anthu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 36