Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 36:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Elihu nabwereza, nati,

2. Mundilole pang'ono, ndidzakuuzani,Pakuti ndiri naonso mau akunenera Mulungu.

3. Ndidzatenga nzeru zanga kutali,Ndidzabvomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama.

4. Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza,Wakudziwitsa mwangwiro ali nanu.

5. Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu, ndipo sapeputsa munthu;Mphamvu ya nzeru zace ndi yaikuru.

6. Sasunga woipa akhale ndi moyo,Koma awaninkha ozunzikazowayenera iwo.

7. Sawacotsera wolungama maso ace,Koma pamodzi ndi mafumu pa mpando waoAwakhazika cikhazikire, ndipo akwezeka.

8. Ndipo akamangidwa m'nsinga,Nakakodwa ndi zingwe za mazunzo,

9. Pamenepo awafotokozera nchito zao,Ndi zolakwa zao, kuti anacita modzikuza.

10. Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize,Nawauza abwerere kuleka mphulupulu.

11. Akamvera ndi kumtumikira,Adzatsiriza masiku ao modala,Ndi zaka zao mokondwera.

Werengani mutu wathunthu Yobu 36