Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 34:31-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu,Ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwa?

32. Cimene sindiciona mundilangize ndi Inu,Ngati ndacita cosalungama sindidzabwerezanso.

33. Kodi cilango ca Mulungu cikhale monga mucifuna inu, pakuti mucikana?Musankhe ndi inu, ine ai;M'mwemo monga mudziwa, nenani.

34. Anthu ozindikira adzanena nane,Inde anthu anzeru onse akundimva adzati,

35. Yobu alankhula wopanda kudziwa,Ndi mau ace alibe nzeru.

36. Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha,Cifukwa ca kuyankha kwace monga anthu amphulupulu,

37. Pakuti pa kucimwa kwace aonjeza kupikisana ndi Mulungu,Asansa manja pakati pa ife,Nacurukitsa maneno ace pa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 34