Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 34:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndithu zoonadi, Mulungu sangacite coipa,Ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.

13. Anamuikiza dziko lapansi ndani?Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?

14. Akadzikumbukila yekha mumtima mwace,Akadzisonkhanitsira yekha mzimu wace ndi mpweya wace,

15. Zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,Ndi munthu adzabwerera kupfumbi.

16. Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ici,Cherera khutu kunena kwanga.

17. Kodi munthu woipidwa naco ciweruzo adzalamulira?Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?

18. Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pace iwe,Kapena kwa akalonga, Oipa inu?

19. Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga,Wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka?Pakuti onsewo ndiwo nchito ya manja ace.

20. M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku,Anthu agwedezeka, napita,Amphamvu acotsedwa opanda dzanja lakuwacotsa.

21. Pakuti maso ace ali pa njira ya munthu ali yense,Napenya moponda mwace monse.

22. Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa,Kuti ocita zopanda pace abisaleko.

23. Pakuti Mulungu alibe cifukwa ca kulingiriranso za munthu,Kuti afike kwa. Iye kudzaweruzidwa.

24. Aphwanya eni mphamvu osaturutsa kubwalo mlandu wao,Naika ena m'malo mwao.

25. Pakuti asamalira nchito zao,Nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.

Werengani mutu wathunthu Yobu 34