Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 34:10-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cifukwa cace mundimvere ine, eni nzeru inu,Nkutali ndi Mulungu kucita coipa,Ndi Wamphamvuyonse kucita cosalungama.

11. Pakuti ambwezera munthu monga mwa nchito yace,Napezetsa munthu ali yense monga mwa mayendedwe ace.

12. Ndithu zoonadi, Mulungu sangacite coipa,Ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.

13. Anamuikiza dziko lapansi ndani?Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?

14. Akadzikumbukila yekha mumtima mwace,Akadzisonkhanitsira yekha mzimu wace ndi mpweya wace,

15. Zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,Ndi munthu adzabwerera kupfumbi.

16. Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ici,Cherera khutu kunena kwanga.

17. Kodi munthu woipidwa naco ciweruzo adzalamulira?Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?

18. Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pace iwe,Kapena kwa akalonga, Oipa inu?

19. Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga,Wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka?Pakuti onsewo ndiwo nchito ya manja ace.

20. M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku,Anthu agwedezeka, napita,Amphamvu acotsedwa opanda dzanja lakuwacotsa.

21. Pakuti maso ace ali pa njira ya munthu ali yense,Napenya moponda mwace monse.

22. Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa,Kuti ocita zopanda pace abisaleko.

23. Pakuti Mulungu alibe cifukwa ca kulingiriranso za munthu,Kuti afike kwa. Iye kudzaweruzidwa.

24. Aphwanya eni mphamvu osaturutsa kubwalo mlandu wao,Naika ena m'malo mwao.

25. Pakuti asamalira nchito zao,Nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.

26. Awakantha ngati oipa,Poyera pamaso pa anthu.

27. Popeza anapambuka, naleka kumtsata,Osasamalira njira zace ziri zonse.

28. M'mwemo anafikitsa kwa Iye kupfuula kwa osauka;Ndipo anamva Iye kupfuula kwa ozunzika.

29. Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani?Akabisa nkhope yace adzampenyerera ndani?Cikacitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, ncimodzimodzi;

30. Kuti munthu wonyoza Mulungu asacite ufumu,Ndi anthu asakodwe mumsampha,

Werengani mutu wathunthu Yobu 34