Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 34:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,

2. Tamverani mau anga, inu anzeru;Mundicherere khutu inu akudziwa.

3. Pakuti khutu liyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya.

4. Tidzisankhire coyeneraco,Tidziwe mwa tokha cokomaco.

5. Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,Ndipo Mulungu wandicotsera coyenera ine.

6. Kodi ndidzinamizire?Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwa.

7. Wakunga Yobu ndani,Wakumwa mwano ngati madzi?

8. Wakutsagana nao ocita mphulupulu,Nayendayenda nao anthu oipa.

9. Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nakoKubvomerezana naye Mulu ngu.

10. Cifukwa cace mundimvere ine, eni nzeru inu,Nkutali ndi Mulungu kucita coipa,Ndi Wamphamvuyonse kucita cosalungama.

Werengani mutu wathunthu Yobu 34