Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 33:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndine woyera ine, wopanda kulakwa,Ndine wosaparamula, ndiribe mphulupulu.

10. Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo,Andiyesa mdani wace;

11. Amanga mapazi anga m'zigologolo,Ayang'anira poyenda ine ponse.

12. Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama;Pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.

13. Mutsutsana ndi Iye cifukwa ninji?Popeza pa zace zonse saulula cifukwa.

14. Pakuti Mulungu alankhula kamodzi,Kapena kawiri, koma anthu sasamalira.

15. M'kulota, m'masomphenya a usiku,Pakuwagwera anthu tulo tatikuru,Pogona mwacheru pakama,

16. Pamenepo atsegula makutu a anthu,Nakomera cizindikilo cilangizo cao;

17. Kuti acotse munthu ku cimene akadacita,Ndi kubisira munthu kudzikuza kwace;

18. Kuti amletse angaonongeke,Ndi moyo wace ungatayike ndi lupanga.

19. Alangidwanso ndi zowawa pakama pace,Ndi kulimbana kowawa kosapuma m'mafupa ace.

20. M'mwemo mtima wace ucita mseru ndi mkate,Ndi moyo wace pa cakudya colongosoka.

Werengani mutu wathunthu Yobu 33