Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 33:24-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pamenepo Mulungu amcitira cifundo, nati,Mlanditse, angatsikire kumanda,Ndampezera dipo.

25. Mnofu wace udzakhala se, woposa wa mwana;Adzabwerera ku masiku a ubwana wace.

26. Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima;M'mwemo aona nkhope yace mokondwera;Ndipo ambwezera munthu cilungamo cace.

27. Apenyerera anthu, ndi kuti,Ndinacimwa, ndaipsa coongokaco,Ndipo sindinapindula nako.

28. Koma anandiombola ndingatsikire kumanda,Ndi moyo wanga udzaona kuunika.

29. Taona, izi zonse azicita MulunguKawiri katatu ndi munthu,

30. Kumbweza angalowe kumanda,Kuti kuunika kwa moyo kumuwalire.

31. Cherani khutu, Yobu, mundimvere ine;Mukhale cete, ndipo ndidzanena ine.

32. Ngati muli nao mau mundiyankhe.Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani.

33. Ngati mulibe mau, tamverani Ine;Mukhale cete, ndipo ndizakuphunzitsani nzeru.

Werengani mutu wathunthu Yobu 33