Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 33:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Komatu, Yobu, mumvere maneno anga,Mucherere khutu mau anga.

2. Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga,Lilime langa lanena m'kamwa mwanga.

3. Maneno anga aulula ciongoko ca mtima wanga,Ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.

4. Mzimu wa Mulungu unandilenga,Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.

5. Ngati mukhoza, mundiyankhe;Mulongosolere mau anu pamaso panga, mukonzeke.

6. Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu;Inenso ndinaumbidwa ndi dothi,

7. Taonani, kuopsa kwanga simudzacita nako mantha;Ndi ici ndikusenzetsani sicidzakulemererani.

8. Zedi mwanena m'makutu mwanga,Ndinamvanso mau akunena kwanu, akuti,

9. Ndine woyera ine, wopanda kulakwa,Ndine wosaparamula, ndiribe mphulupulu.

10. Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo,Andiyesa mdani wace;

11. Amanga mapazi anga m'zigologolo,Ayang'anira poyenda ine ponse.

12. Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama;Pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 33