Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 32:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cifukwa cace ndinati, Ndimvereni ine,Inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine.

11. Taonani, ndinalindira mau anu,Ndinacherera khutu zifukwa zanu,Pofunafuna inu ponena.

12. Inde ndinasamalira inu;Koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu,Kapena wakumbwezera mau pakati painu.

13. Msamati, Tapeza nzeru ndife,Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai;

14. Popeza sanandiponyera ine mau,Sindidzamyankha ndi maneno anu.

15. Asumwa, sayankhanso, Anawathera mau.

16. Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo,Popeza akhala du osayankhanso?

17. Ndidzayankha inenso mau anga,Ndidzaonetsa inenso za m'mtima mwanga.

18. Pakuti ndadzazidwa ndi mau,Ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza.

19. Taonani, m'cifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira,Ngati matumba atsopano akuti aphulike.

20. Ndidzanena kuti cifundo citsike;Ndidzatsegula milomo yanga ndi kuyankha.

21. Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu,Kapena kumchula munthu maina omdyola nao;

22. Pakuti sindidziwa kuchula maina osyasyalika;Ndikatero Mlengi wanga adzandicotsa msanga.

Werengani mutu wathunthu Yobu 32