Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 31:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,Ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,

10. Mkazi wanga aperere wina;Wina namuike kumbuyo.

11. Pakuti ico ndi coipitsitsa,Ndico mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wace.

12. Pakuti ndico moto wakunyeka mpaka cionongeko,Ndi cakuzula zipatso zanga zonse.

13. Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga,Potsutsana nane iwo,

14. Ndidzatani ponyamuka Mulungu?Ndipo pondizonda Iye ndidzamyankha ciani?

15. Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenga iyenso?Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?

16. Ngati ndakaniza aumphawi cifuniro cao,Kapena kutopetsa maso a amasiye,

17. Kapena kudya nthongo yanga ndekha,Osadyako mwana wamasiye;

18. (Pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate;Ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye cibadwire ine.)

Werengani mutu wathunthu Yobu 31