Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 31:28-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Icinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wace;Pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.

29. Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,Kapena kudzitukula pompeza coipa;

30. Ndithu sindinalola m'kamwa mwanga mucimwe,Kupempha motemberera moyo wace.

31. Ngati amuna a m'hema mwanga sanati,Ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?

32. Mlendo sakagona pakhwalala,Koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.

33. Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu,Ndi kubisa mphulupulu yanga m'cifuwa mwanga;

34. Popeza ndinaopa unyinji waukuru,Ndi cipepulo ca mapfuko cinandiopsetsa;Potero ndinakhala cete osaturuka pakhomo panga.

35. Ha! ndikadakhala naye wina wakundimvera,Cizindikilo canga sici, Wamphamvuyonse andiyankhe;Mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wangal

36. Ndithu ndikadawasenza paphewa panga,Ndi kudzimangirira awa ngati korona.

37. Ndikadamfotokozera ciwerengo ca mopondamo mwanga,Ndikadamsenderera Iye ngati ka longa,

38. Ngati minda yanga ipfuula monditsutsa,Ndi nthumbira zace zilira pamodzi;

39. Ngati ndadya zipatso zace wopanda ndarama,Kapena kutayitsa eni ace moyo wao;

40. Imere minga m'malo mwa tirigu,Ndi dawi m'malo mwa barele.Mau a Yobu atha.

Werengani mutu wathunthu Yobu 31