24. Ngati ndayesa golidi ciyembekezo canga,Ndi kunena ndi golidi woyengetsa,Ndiwe cikhazikitso canga;
25. Ngati ndinakondwera popeza cuma canga ncacikuru,Ndi dzanja langa lapeza zocuruka;
26. Ngati ndalambira dzuwa lirikuwala,Kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;
27. Ndi mtima wanga wakopeka m'tseri,Ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;
28. Icinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wace;Pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.
29. Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,Kapena kudzitukula pompeza coipa;
30. Ndithu sindinalola m'kamwa mwanga mucimwe,Kupempha motemberera moyo wace.
31. Ngati amuna a m'hema mwanga sanati,Ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?
32. Mlendo sakagona pakhwalala,Koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.