Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 31:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ngati zuuno zace sizinandiyamika,Ngati sanapfunda ubweya wa nkhosa zanga;

21. Ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,Popeza ndinaona thandizo langa kucipata;

22. Libanthuke phewa langa paphalo,Ndi dzanja langa liduke pagwangwa.

23. Pakuti tsoka locokera kwa Mulungu linandiopsa,Ndi cifukwa ca ukulu wace sindinakhoza kanthu,

24. Ngati ndayesa golidi ciyembekezo canga,Ndi kunena ndi golidi woyengetsa,Ndiwe cikhazikitso canga;

25. Ngati ndinakondwera popeza cuma canga ncacikuru,Ndi dzanja langa lapeza zocuruka;

26. Ngati ndalambira dzuwa lirikuwala,Kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;

27. Ndi mtima wanga wakopeka m'tseri,Ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;

28. Icinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wace;Pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.

29. Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,Kapena kudzitukula pompeza coipa;

30. Ndithu sindinalola m'kamwa mwanga mucimwe,Kupempha motemberera moyo wace.

31. Ngati amuna a m'hema mwanga sanati,Ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?

Werengani mutu wathunthu Yobu 31