Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 31:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinapangana ndi maso anga,Potero ndipenyerenji namwali?

2. Pakuti gawo la Mulungu locokera kumwamba,Ndi colowa ca Wamphamvuyonse cocokera m'mwambamo nciani?

3. Si ndizo cionongeko ca wosalungama,Ndi tsoka la ocita mphulupulu?

4. Nanga sapenyanjira zanga,Ndi kuwerenga moponda mwanga monse?

5. Ngati ndinayanjana nalo bodza,Ndi phazi langa linathamangira cinyengo;

6. Andiyese ndi muyeso wolingana,Kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.

7. Ngati phazi langa linapambuka m'njira,Ndi mtima wanga unatsata maso anga?Ngati cirema camamatira manja anga?

8. Ndibzale ine nadye wina,Ndi zondimerera ine zizulidwe.

9. Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,Ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,

10. Mkazi wanga aperere wina;Wina namuike kumbuyo.

11. Pakuti ico ndi coipitsitsa,Ndico mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wace.

12. Pakuti ndico moto wakunyeka mpaka cionongeko,Ndi cakuzula zipatso zanga zonse.

13. Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga,Potsutsana nane iwo,

14. Ndidzatani ponyamuka Mulungu?Ndipo pondizonda Iye ndidzamyankha ciani?

15. Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenga iyenso?Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?

16. Ngati ndakaniza aumphawi cifuniro cao,Kapena kutopetsa maso a amasiye,

Werengani mutu wathunthu Yobu 31