8. Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;Anawaingitsa kuwacotsa m'dziko.
9. Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo,Nandiyesa nthanthi.
10. Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine,Saleka kuthira malobvu pankhope panga.
11. Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza;Anataya comangira m'kamwa mwao pamaso panga.
12. Ku dzanja langa lamanja anauka oluluka,Akankha mapazi anga,Andiundira njira zao zakundiononga.
13. Aipsa njira yanga,Athandizana ndi tsoka langa;Ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.