Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 30:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Atsala mafupa okha okha ndi kusowa ndi njala;Akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'cipululu copasuka.

4. Achera terere lokolera kuzitsamba,Ndi cakudya cao ndico mizu ya dinde.

5. Anawapitikitsa pakati pa anthu,Awapfuulira ngati kutsata mbala.

6. Azikhala m'zigwa za cizirezire,M'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga.

7. Pakati pa zitsamba alira ngati buru,Pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.

8. Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;Anawaingitsa kuwacotsa m'dziko.

Werengani mutu wathunthu Yobu 30