Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 30:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mphamvunso ya m'manja mwao ndikadapindulanji nayo?Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha,

3. Atsala mafupa okha okha ndi kusowa ndi njala;Akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'cipululu copasuka.

4. Achera terere lokolera kuzitsamba,Ndi cakudya cao ndico mizu ya dinde.

5. Anawapitikitsa pakati pa anthu,Awapfuulira ngati kutsata mbala.

6. Azikhala m'zigwa za cizirezire,M'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga.

Werengani mutu wathunthu Yobu 30