Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 30:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Iye anandiponya m'matope,Ndipo ndafanana ndi pfumbi ndi phulusa.

20. Ndipfuula kwa Inu, koma simundiyankha;Ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.

21. Mwasandulika kundicitira nkharwe;Ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.

22. Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo;Ndipo mundisungunula mumkuntho.

23. Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,Ndi ku nyumba yokomanamo amoyo onse.

24. Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lace kodi?Akati aonongeke, sapfuulako kodi?

25. Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa?Kodi moyo wanga sunacitira cisoni osowa?

26. Muja ndinayembekeza cokoma cinadza coipa,Ndipo polindira kuunika unadza mdima.

27. M'kati mwanga mupweteka mosapuma,Masiku a mazunzo andidzera.

28. Ndiyenda ndiri wothimbirira osati ndi dzuwa ai;Ndinyamuka mumsonkhano ndi kupfuula,

Werengani mutu wathunthu Yobu 30