Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 3:22-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Wakusekerera ndi cimwemweNdi kukondwera pakupeza manda?

23. Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika,Amene wamtsekera Mulungu?

24. Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga;Ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.

25. Pakuti cimene ndinaciopa candigwera,Ndi cimene ndacita naco mantha candidzera.

26. Wosakhazikika, ndi wosakhala cete, ndi wosapumula ine,Koma mabvuto anandidzera.

Werengani mutu wathunthu Yobu 3