Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 3:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Kapena pamodzi ndi akalonga eni ace a golidi,Odzaza nyumba zao ndi siliva;

16. Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zi;Ngati makanda osaona kuunika.

17. Apo oipa aleka kumabvuta;Ndi apo ofoka mphamvu akhala m'kupumula.

18. Apo a m'kaidi apumula pamodzi,Osamva mau a wofulumiza wao.

19. Ang'ono ndi akulu ali komwe;Ndi kapolo amasuka kwa mbuyace.

20. Amninkhiranji kuunika wobvutika,Ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,

21. Wakuyembekezera imfa, koma kuli zi,Ndi kuikumba koposa cuma cobisika,

Werengani mutu wathunthu Yobu 3